1

1 KATUNDU wa Nineve. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

2 Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera cilango; Yehova ndiye wobwezera cilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera cilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ace.

3 Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikuru; ndi wosamasula ndithu woparamula; njira ya Yehova iri m'kabvumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo pfumbi la mapazi ace.

4 Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basana ndi Karimeli afota, ndi duwa la ku Lebano linyala.

5 Mapiri agwedezeka cifukwa ca Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pace, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.

6 Adzaima ndani pa kulunda kwace? ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wace wotentha? ukali wace utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.

7 Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.

8 Koma ndi cigumula cosefukira adzatha konse malo ace, nadzapitikitsira adani ace kumdima.

9 Mulingaliranji cotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.

10 Pakuti cinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera naco coledzeretsa cao, adzathedwa konse ngati ciputu couma.

11 Mwa iwe waturuka wina wolingalira coipa cotsutsana ndi Yehova, ndiye phungu wopanda pace.

12 Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nacuruka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Cinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso.

13 Koma tsopano ndidzatyola ndi kukucotsera goli lace, ndipo ndidzadula zomangira zako.

14 Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzacotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.

15 Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! cita madyerero ako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda paceyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.

2

1 Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'cuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.

2 Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wace wa Yakobo ngati ukulu wace wa Israyeli; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zace za mpesa.

3 Zikopa za amphamvu ace zasanduka zofiira, ngwazi zibvala mlangali; magareta anyezimira ndi citsulo tsiku la kukonzera kwace, ndi mikondo itinthidwa.

4 Magareta acita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.

5 Akumbukila omveka ace; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira ku linga lace, ndi cocinjiriza cakonzeka.

6 Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi cinyumba casungunuka.

7 Catsimikizika, abvulidwa, atengedwa, adzakazi ace alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pacifuwa pao.

8 Koma Nineve wakhala ciyambire cace ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! ati, koma palibe woceuka.

9 Funkhani siliva, funkhani golidi; pakuti palibe kutha kwace kwa zosungikazo, kwa cuma ca zipangizo zofunika ziri zonse.

10 Ndiye mopanda kanthu mwacemo ndi mwacabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.

11 Iri kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango; kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?

12 Mkangowo unamwetula zofikira ana ace, nusamira yaikazi yace, nudzaza mapanga ace ndi nyama, ngaka zace ndi zojiwa.

13 Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magareta ace m'utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzacotsa zofunkha zako pa dziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.

3

1 Tsoka mudzi wa mwazi! udzala nao mabodza ndi zacifwamba; zacifwamba sizidukiza.

2 Kumveka kwa cikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magareta; ndi kaphata kaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magareta;

3 munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi cimulu ca mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;

4 cifukwa ca ciwerewere cocuruka ca waciwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsa amitundu mwa ciwerewere cace, ndi mabanja mwa nyanga zace.

5 Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsaru yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umarisece wako, ndi maufumu manyazi ako.

6 Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukucititsa manyazi, ndi kukuika copenyapo,

7 Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Nineve wapasuka, adzamlira maliro ndani? ndidzakufunira kuti akukutonthoza?

8 Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pa mitsinje wozingidwa ndi madzi; amene chemba lace ndilo nyanja, ndi linga lace ndilo nyanja?

9 Kusi ndi Aigupto ndiwo mphamvu yace, ndiyo yosatha, Puti ndi Lubimu ndiwo akukuthandiza.

10 Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ace a makanda anaphwanyika polekeza pace pa miseu yace yonse; ndi pa omveka ace anacita maere, ndi akulu ace onse anamangidwa maunyolo.

11 Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira cifukwa ca mdani.

12 Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akaigwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya.

13 Taona, anthuako m'kati mwako akunga akazi; zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakuru; moto watha mipingiridzo yako.

14 Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.

15 Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati cirimamine; udzicurukitse ngati cirimamine, udzicurukitse ngati dzombe.

16 Wacurukitsa amalonda ako koposa nyenyezi za kuthambo; cirimamine anyambita, nauluka, nathawa.

17 Obvala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazembe ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'macinga tsiku lacisanu, koma likafundukula dzuwa ziuluka nizithawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.

18 Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asuri; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.

19 Palibe cakulunzitsa kutyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?